DZINA_________________________________________________________________________
NORTHERN EDUCATION DIVISION
  2025 MALAWI SCHOOL CERTIFICATE MOCK EXAMINATIONS
                                      CHICHEWA
                                                                Subject Number: M039/III
Monday, 7 April                                                      Time Allowed:2 hrs
                                                                        8:00-10:00 am
                                        PAPER III
                                         (Malikisi 70)
Malangizo
   1. Onetsetsani kuti pepala ili lili ndi             Funso    Chongani      Muno
                                                                funso ngati   musalembemo
      masamba osindikizidwa khumi
                                                                mwayankha
                                                            1
   2. Pepalali lili ndi magawo awiri: A ndi B.
                                                            2
   3. Lembani dzina lanu pamwamba pa                        4
      tsamba lililonse la pepalali.
   4. Muchitebulo chili kumbaliku onetsani funso
      lililonse lomwe mwayankha pochonga
      mubokosi lomwe lili kutsogolo kwake.
   5. Perekani pepala lanu kwa
      oyang’anira mayeso nthawi ikakwana.
                                             Page 1 of 11
DZINA_________________________________________________________________________
                                 Gawo A (Malikisi 30)
                         Nkhani za Mchezo ndi Zolembedwa
   Langizo: Yankhani mafunso onse m’gawoli pa mizere ili pansi pa funso lililonse.
   1. Werengani ndakatulo ili m’munsimu ndipo muyankhe mafunso otsatirawo.
      BWERERANI (Wokomaatani Malunga)
      Munasiya Yokoniya
      Akulima Kilombero
      Ku dambo kugwiritsa
      Ntchito nzeru anakapeza
      Ku sekondale m’mbuyomu
      Nkumati mmene mwaphunziramo
      Khasu ayi koma cholembera
      Mmanja taye ili petupetu
      Pa kholingo ku Kabula.
      M’manyoza Gamaliyeli
      Wosodza milamba ndi mphuta
      Nkumapeza chuma
      Cholimira mbewu za kudimba
      Zomulola ngati zamulawula
      Nkumati akuseweretsa
      Dipuloma pomakhala nayo m’mudzi
      Ku Ndirande nduko mwafika
      Nanga mukutani pachiguduli
      Mwayesa mphasa anzanga?
      Gamaliyeli akupha mkonono
      Pa kama ogula yekha
      Matilesi ali wofuwofu
      Mtsamiro wa makono
      Utasunga mutu wake.
      Nkakhumbi ka zipepala
      Za pulasitiki mukuchitamonji?
      Yokoniya ali m’nyumba yolozeka
      Ya malata ndi njerwa zogula yekha
      Kilombero wadzamtengezeni atakolola
      Mumanamizana kudya galu
      Kuyesa ndiwo ndi bwenzi lako.
      Kusenza matumba pamsika
      Si ukalaliki olemba matikiti
                                      Page 2 of 11
DZINA_________________________________________________________________________
      Ndinkona ukulakalaka nsima yoyera
      Mgaiwa wa mkalaya utakumera.
      Ndiyetu lero iwe bwevuka
      Ku tawuni ukuchedwako
      Dzalime soya odyetsa nkhuku
      Akugule anthu akasamalire ziweto
      Vomera unkatsata opanda madzi
      Tikulandire ku mudzi kuno.
      Udayipitsa pamsasa pochoka zowona.
      Koma kukhululuka ndiye kwathu
      Poti munthu salakwira mtengo.
      usawope kusekedwa tonse timachimwa
      Minda njatayetaye kuno.
      Polima sudzapasowa.
      Kanthu mkhama dziwa.
      Chuma chili m’nthakamu.
      Wophunzira wonga iwe
      Sangasowe kogulitsa zowundukula.
      Dzaphe chuma ndi Yokoniya komanso Gamaliyeli.
      Mafunso
      a. Ndani akuyankhula mu ndakatuloyi?
          __________________________________________________________________
                                                                         (Malikisi 1)
      b. Kodi woyankhula mu ndakatuloyi akuyankhula ndi ndani?
          __________________________________________________________________
                                                                         (Malikisi 1)
      c. Tsimikizira kuti woyankhulidwa mu ndakatuloyi akuvutika komwe aliko?
          __________________________________________________________________
          __________________________________________________________________
                                                                         (Malikisi 2)
      d. Tchulani kamvekedwe ka zoyankhula m’ndakatuloyi.
          __________________________________________________________________
                                                                         (Malikisi 1)
      e. Perekani zitsanzo ziwiri za zipangizo zotsatirazi:
         (i)    mkuluwiko
                                       Page 3 of 11
DZINA_________________________________________________________________________
             __________________________________________________________________
             __________________________________________________________________
                                                                     (Malikisi 2)
             (ii)      mvekero

             (iii)     chithunzithunzi
             __________________________________________________________________
             __________________________________________________________________
                                                                              (Malikisi 2)
             (iv)      chining’a
                     _______________________________________________________________
                     _______________________________________________________________
                                                                              (Malikisi 2)
        f. Perekani phunziro lomwe mwapeza mu ndakatuloyi.
             __________________________________________________________________
             __________________________________________________________________
                                                                              (Malikisi 2)
   2. Werengani nkhani ili m’munsimu mosamala ndipo muyankhe mafunso otsatirawo.
                              KUSANKHA CHINTHU CHIMODZI
M’mudzi wina munali banja lina limene linali ndi chuma chambiri choposa chimene maanja
ena onse anali nacho m’mudzimo. Banjalo linali ndi nyumba zabwino, ng’ombe, nkhokwe za
zakudya ndi zovala zambiri ndipo silinkasowa kanthu. Banja la chumalo linali lamakhalidwe
abwino kwambiri ndipo linali ndi abwenzi ambiri amene ankalikonda chifukwa cha mtima
wofuna kukhala bwino ndi munthu aliyense.
Bambo     ndi        mayi   olemerawo    anali   ndi   mwana   wamwamuna   mmodzi   amene
ankamukhulupilira kwambiri. Anthuwo anali ndi wantchito wamwamuna mmodzi amene
anakhala naye zaka zambiri ndipo wantchitoyo ankangokhala ngati mwana wachisamba
wabanjalo.
                                             Page 4 of 11
DZINA_________________________________________________________________________
Chaka china mwamuna wolemera uja anayamba kudwala. Tsiku lina matenda anafika povuta
kwambiri ndipo bambo uja anakhala ndi banja lake ndipo kenako anapemphera pamene
anaona kuti anali pafupi kutsirizika chifukwa anali wokalamba kwambiri. Atatha pemphero
lake, iye ananena kuti zoonadi anali munthu wamvula zakale ndiponso anali wachuma
chambiri. Anati chomwe anafuna chinali choti akamwalira, chuma chake chonse
chidzapatsidwe kwa wantchito wake osati kwa mwana kapena mkazi wake ayi. Komabe iye
anati mwana wakeyo adzaloledwe kusankha chinthu chimodzi chokha basi ndipo zonse
zotsala zidzakhale za wantchito. Izi zinadabwitsa kwambiri mwana ndi mkazi wake.
Patapita tsiku limodzi, mwamuna uja anamwalira ndipo dera lonse lija linalira maliro
momvetsa chisoni chifukwa cha maliro a wokondedwa wawo. Anthu ambiri analiranso
kwambiri atamva zomwe malemuwo ananena zokhudza chuma chake.
Nthawi yolira maliro itatha, mnyamata uja anayamba kukhala ndi maganizo ambiri popeza
sanadziwe chinthu chimodzi chokha chomwe iye anayenera kusankha. Chifukwa cha kudya
mutu nthawi yaitali, iye anayamba kuwonda kwambiri ndipo ankangokhalira kudandaula kuti
chuma chake chipita kwa munthu wadera.
Tsiku lina mnyamatayo akuyenda m’njira chifukwa chosowa zochita, anaona mayi wina
wokalamba wa m’mudzimo atasenza katundu. Mnyamatayo anamuthangata mayi wokalamba
uja pomunyamulira katundu wake mpaka kukamufikitsa kunyumba kwake. Asanabwerere
kwawo, mayi wokalamba uja anamufunsa mnyamatayo chifukwa chomwe ankakhalira
wosungulumwa komanso chomwe chinkamuondetsa. Mnyamata uja analongosola za
chomwe chinkamudya moyo wake. Mayi uja anamuuza mnyamata uja chomwe iye anayenera
kusankha mmalo mwa zonse. Atamva malangizowo, m’nyamata anayamba kusangalala
chifukwa anapeza chosankha chabwino.
Tsiku losankha chinthu chimodzi litakwana, kunyumba kunasonkhana khwimbi la anthu bii
omwe anafuna kuona chomwe mnyamata uja asankhe poti chuma chonse chija chinali cha
wantchito uja osati mnyamatayo kapena amake.
Bungwe la anthu omwe ankayendetsa mwambo woti mnyamata uja asankhe chinthu
chimodzi, linamuuza mnyamata kuti asankhe chinthu cha kumtima kwake.
                                       Page 5 of 11
DZINA_________________________________________________________________________
Wapampando wagululo anati, “nthawi yakwana, yoti usankhe chinthu chimodzi. Tsopano
sankha chinthu chimodzi monga momwe ananenera malemu bambo ako.”
Mnyamatayo anamwetulira ndipo anati, “Ndilibe chosankha china; ndasankha wantchitoyu.
Zikomo kwambiri.”
Anthu onse anazizwa ndi nzeru za mnyamatayo ndipo anasangalala kwambiri.
Tsopano yankhani mafunso otsatirawa.
   (a) Nkhaniyi ikuchitira kuti?
      _____________________________________________________________________
                                                                           (Malikisi 1)
   (b) Ndi khalidwe lotani lomwe mwini chuma adawonetsa kwa wantchito wake?
      _____________________________________________________________________
                                                                           (Malikisi 1)
   (c) Tchulani mphendero ya nkhaniyi.
      _____________________________________________________________________
                                                                           (Malikisi 1)
   (d) Tsimikizani kuti mwana wa mwinichuma adali waulemu.
      _____________________________________________________________________
      _____________________________________________________________________
                                                                           (Malikisi 2)
   (e) Kuchokera mu nkhaniyi, perekani zipangizo zitatu ndi chitsanzo pa chipangizo
      chilichonse.
      (i)     _______________________________________________________________
              _______________________________________________________________
                                                                           (Malikisi 2)
      (ii)    _______________________________________________________________
              _______________________________________________________________
                                                                           (Malikisi 2)
                                         Page 6 of 11
DZINA_________________________________________________________________________
      (iii)      _______________________________________________________________
                 _______________________________________________________________
                                                                                (Malikisi 2)
   (f) Pezani matanthauzo a mawu otsatirawa:
              (ii)kudya mutu
              _________________________________________________________________
                                                                                (Malikisi 2)
              (iii)chinkamudya moyo
              _________________________________________________________________
                                                                                (Malikisi 2)
                                          Gawo B (Malikisi 40)
Langizo: Yankhani mafunso awiri okha m’gawoli m’ndime zofotokozedwa bwino.
                                  NTHONDO (S J Nthala)
   3. (a)        Tsimikizani popereka mfundo zinayi zosonyeza kuti atengambali ena anali
                 osamala udindo wawo mu nthanoyi.
                                                                              (Malikisi 40)
                                      KAPENA
      (a)        Nthondo anali wolimba mtima. Fotokozani mfundo zinayi.
                                                                              (Malikisi 40)
___________________________________________________________________________

                                         Page 7 of 11

                                   Page 8 of 11

                              CHAMDOTHE NDI ZISUDZO ZINA
                                    (S Likongwe, W Nkhoma)
                                        ZIKANI
   4. (a)   Tsimikizani popereka mfundo zinayi kuti atengambali ena amaphwanyiridwa
            ufulu mu chisudzo cha Zikani.
                                                                       (Malikisi 40)
                                            KAPENA
                                     Page 9 of 11
DZINA_________________________________________________________________________
                            MUDZI WA MFUMU TANDWE
      (b)   Fotokozani mfundo zinayi zomwe zikupezeka mu chisudzo cha Mudzi wa
            Mfumu Tandwe.

                                  Page 10 of 11

                    MAFUNSO ATHERA PANO
                                  Page 11 of 11